-
2 Mafumu 9:6, 7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Choncho Yehu ananyamuka nʼkulowa mʼnyumba. Ndiyeno mtumiki wa mneneri uja anatenga mafuta aja nʼkumuthira pamutu. Kenako anamuuza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ndikukudzoza kuti ukhale mfumu ya anthu a Yehova, Aisiraeli.+ 7 Ukaphe anthu a mʼbanja la mbuye wako Ahabu ndipo ine ndidzabwezera magazi a atumiki anga aneneri ndiponso magazi a atumiki onse a Yehova amene Yezebeli anawapha.+
-