-
2 Mafumu 11:1-3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Ataliya,+ mayi ake a Ahaziya ataona kuti mwana wawo wafa,+ anapha anthu onse amene anali oyenera kulowa ufumu.*+ 2 Koma Yehoseba mwana wamkazi wa Mfumu Yehoramu, mchemwali wake wa Ahaziya, anaba Yehoasi+ mwana wamwamuna wa Ahaziya, pagulu la ana aamuna a mfumu amene ankayenera kuphedwa. Anatenga Yehoasi ndi mayi amene ankamusamalira nʼkukawaika mʼchipinda chamkati chogona. Anakwanitsa kubisa mwanayo kuti Ataliya asamuone, moti sanaphedwe. 3 Anakhalabe ndi mayi womusamalirayo mʼnyumba ya Yehova mmene anamubisa kwa zaka 6, pamene Ataliya ankalamulira dzikolo.
-