-
2 Mafumu 11:5-8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Ndiyeno anawalamula kuti: “Muchite izi: Mukhale mʼmagulu atatu ofanana ndipo gulu limodzi lidzabwere pa tsiku la Sabata kudzalondera nyumba yachifumu mosamala.+ 6 Gulu lina lidzakhale pageti lotchedwa Maziko ndipo gulu lachitatu lidzakhale pageti kumbuyo kwa asilikali olondera nyumba yachifumu. Muzidzasinthana kulondera nyumbayo. 7 Magulu awiri amene anayenera kupuma pa Sabata asadzachoke. Onsewa adzalondere mosamala nyumba ya Yehova poteteza mfumu. 8 Mudzazungulire mfumuyo kumbali zonse mutatenga zida ndipo aliyense wofuna kudutsa pakati panu, adzaphedwe. Muzidzateteza mfumuyo kulikonse kumene ingapite.”
-
-
1 Mbiri 9:22-25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Onse amene anasankhidwa kuti akhale alonda apamakomo analipo 212. Iwo ankakhala mʼmidzi yawo mogwirizana ndi mndandanda wa mayina wotsatira makolo awo.+ Davide ndi Samueli wamasomphenya+ anaika anthuwa pa udindo wawo chifukwa cha kukhulupirika kwawo. 23 Iwo ndi ana awo ankayangʼanira anthu amene ankachita utumiki wolondera mageti a nyumba ya Yehova kapena kuti chihema chopatulika.+ 24 Alonda apagetiwo ankakhala mbali zonse 4, kumʼmawa, kumadzulo, kumpoto ndi kumʼmwera.+ 25 Nthawi ndi nthawi abale awo amene ankakhala mʼmidzi yawo, ankabwera kudzagwira nawo ntchito kwa masiku 7.
-