-
2 Mafumu 11:9-12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Atsogoleri a magulu a asilikali 100+ anachitadi zimene wansembe Yehoyada analamula. Choncho, aliyense anatenga asilikali ake amene ankagwira ntchito pa Sabata ndi amene ankafunika kupuma pa Sabata, nʼkupita kwa wansembe Yehoyada.+ 10 Wansembeyo anapatsa atsogoleri a magulu a asilikali 100 aja mikondo ndi zishango zozungulira zimene zinali za Mfumu Davide, zomwe zinali mʼnyumba ya Yehova. 11 Asilikali olondera nyumba yachifumu+ anaima pamalo awo, aliyense atanyamula zida zake, kuyambira kumanja kwa nyumbayo mpaka kumanzere kwa nyumbayo, pafupi ndi guwa lansembe+ ndiponso pafupi ndi nyumbayo. Anazungulira mfumuyo kumbali zonse. 12 Kenako Yehoyada anatulutsa mwana wa mfumu+ uja nʼkumuveka chipewa chachifumu nʼkuika mpukutu wa Chilamulo cha Mulungu pamutu pake.+ Choncho anamuveka ufumu nʼkumudzoza. Ndiyeno anayamba kuwomba mʼmanja nʼkumanena kuti: “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!”+
-