14 Ndiyeno Abulahamu anadzuka mʼmawa kwambiri nʼkutenga mkate ndi thumba lachikopa la madzi, ndipo anaziika paphewa pa Hagara. Atatero anamuuza kuti azipita limodzi ndi mwana wakeyo.+ Choncho Hagarayo ananyamuka nʼkumangoyendayenda mʼchipululu cha Beere-seba.+