-
1 Mafumu 7:15-22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Anaumba zipilala ziwiri zakopa.+ Chipilala chilichonse chinali chachitali mikono 18, ndipo kuzungulira chipilala chilichonse inali mikono 12.+ 16 Anapanga mitu iwiri yakopa nʼkuiika pamwamba pa zipilalazo. Mutu umodzi unali wautali mikono 5, ndipo mutu winawo unalinso wautali mikono 5. 17 Pamutu wa chipilala chilichonse anaikapo maukonde opangidwa ndi matcheni opotanapotana.+ Pamutu wina anaikapo ukonde wopangidwa ndi matcheni 7 ndipo pamutu winawo anaikaponso ukonde wopangidwa ndi matcheni 7. 18 Kenako anapanga mizere iwiri ya makangaza* kuzungulira maukonde awiri aja, nʼkuveka mitu imene inali pamwamba pa zipilalazo. Anachita zimenezi pamitu yonse iwiri. 19 Mbali yokwana mikono 4 ya mitu imene inali pamwamba pa zipilala, pafupi ndi khonde, anaipanga ngati maluwa. 20 Mitu iwiriyo inali pamwamba pa zipilala komanso pamwamba pa malo ozungulira amene analumikizira maukonde aja. Kuzungulira mutu uliwonse, panali makangaza 200 amene anali mʼmizere.+
21 Ndiyeno Hiramu anaika zipilala zija pakhonde la kachisi.*+ Chipilala chimodzi anachiika mbali yakumanja* nʼkuchipatsa dzina lakuti Yakini.* Chipilala china anachiika mbali yakumanzere* nʼkuchipatsa dzina lakuti Boazi.*+ 22 Pamwamba pa chipilala chilichonse panali pooneka ngati maluwa. Choncho, anamaliza ntchito yopanga zipilalazo.
-
-
2 Mbiri 4:11-13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Hiramu anapanganso ndowa, mafosholo ndi mbale zolowa.+
Choncho iye anamaliza ntchito imene ankagwirira Mfumu Solomo panyumba ya Mulungu woona.+ 12 Pa ntchitoyi anapanga zipilala ziwiri,+ mitu ya zipilala yooneka ngati mbale zolowa imene anaiika pamwamba pazipilala ziwirizo komanso maukonde awiri+ okutira mitu iwiri imene inali pazipilalazo. 13 Anapanganso makangaza 400+ oika pamaukonde awiri aja ndipo panali mizere iwiri ya makangaza* pa ukonde uliwonse. Makangazawo anali okutira mitu iwiri yooneka ngati mbale zolowa imene inali pazipilala ziwiri zija.+
-
-
Yeremiya 52:22, 23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Mutu wa chipilala chilichonse unali wakopa. Mutuwo unali wautali mamita awiri*+ ndipo maukonde ndi makangaza* amene anazungulira mutuwo, onse anali akopa. Chipilala chachiwiri chinali chofanana ndi choyambacho, chimodzimodzinso makangaza ake. 23 Makangaza amene anali mʼmbali mwa zipilalazo analipo 96 ndipo makangaza onse amene anazungulira maukondewo analipo 100.+
-