34 Koma ansembe anali ochepa kwambiri moti sakanatha kusenda nyama zonse za nsembe zopsereza. Choncho abale awo Alevi anawathandiza+ mpaka pamene ntchitoyo inatha ndiponso pamene ansembewo anadziyeretsa,+ chifukwa Alevi ankaona kuti kudziyeretsa nʼkofunika kwambiri kuposa mmene ansembe ankaonera.