18 Pasika ngati ameneyu anali asanachitikepo mu Isiraeli kuchokera mu nthawi ya mneneri Samueli. Mafumu ena onse a Isiraeli anali asanachitepo Pasika ngati amene anachita Yosiya,+ ansembe, Alevi, Ayuda ndi Aisiraeli onse amene analipo ndiponso anthu a ku Yerusalemu.