25 Pa nthawiyi, Hezekiya anaika Alevi panyumba ya Yehova atanyamula zinganga, zoimbira za zingwe ndi azeze.+ Iwo ankatsatira malamulo oimbira a Davide,+ a Gadi+ yemwe anali wamasomphenya wa mfumu, ndiponso a mneneri Natani,+ chifukwa malamulowo anachokera kwa Yehova kudzera mwa aneneri ake.