-
Ezara 3:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Kenako Yesuwa+ mwana wa Yehozadaki ndi ansembe anzake ndiponso Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli+ ndi abale ake, anakamanga guwa lansembe la Mulungu wa Isiraeli. Anachita zimenezi kuti aziperekerapo nsembe zopsereza, mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼChilamulo cha Mose,+ munthu wa Mulungu woona.
-
-
Ezara 3:8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Mʼchaka chachiwiri kuchokera pamene anabwera kunyumba ya Mulungu woona ku Yerusalemu, mʼmwezi wachiwiri, Zerubabele mwana wa Salatiyeli, Yesuwa mwana wa Yehozadaki, abale awo onse, ansembe ndi Alevi ndiponso anthu ena onse amene anabwera ku Yerusalemu kuchokera ku ukapolo,+ anayamba kugwira ntchito. Anasankha Alevi oyambira zaka 20 kupita mʼtsogolo kuti akhale oyangʼanira ntchito yapanyumba ya Yehova.
-