-
Ezara 5:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Pa nthawi imeneyo Tatenai bwanamkubwa wa kutsidya lina la Mtsinje,* Setara-bozenai ndi anzawo anabwera kwa Ayudawo nʼkuwafunsa kuti: “Kodi ndi ndani wakulamulani kuti mumange nyumbayi komanso kumaliza ntchitoyi?”* 4 Anawafunsanso kuti: “Kodi anthu amene akumanga nyumba imeneyi mayina awo ndi ndani?”
-