14 Akasidiwo anatenganso ndowa, mafosholo, zozimitsira nyale, makapu ndi ziwiya zonse zakopa zimene ansembe ankagwiritsa ntchito potumikira mʼkachisi. 15 Mkulu wa asilikali olondera mfumu uja anatenga zopalira moto ndi mbale zolowa, zomwe zinali zagolide+ komanso zasiliva weniweni.+