-
2 Mbiri 36:22, 23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Mʼchaka choyamba cha Koresi+ mfumu ya Perisiya, pokwaniritsa mawu a Yehova amene analankhula kudzera mwa Yeremiya,+ Yehova analimbikitsa Koresi mfumu ya Perisiya kuti alengeze mu ufumu wake wonse, zomwenso iye analemba mʼmakalata,+ kuti: 23 “Koresi mfumu ya Perisiya wanena kuti, ‘Yehova Mulungu wakumwamba wandipatsa maufumu onse apadziko lapansi.+ Iye wandituma kuti ndimumangire nyumba ku Yerusalemu mʼdziko la Yuda.+ Aliyense amene ali pakati panu mwa anthu onse amene amamutumikira, Yehova Mulungu wake akhale naye ndipo apite.’”+
-
-
Ezara 6:3, 4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 “Mʼchaka choyamba cha Mfumu Koresi, mfumuyo inaika lamulo lokhudza nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu lakuti:+ ‘Ayuda amangenso nyumbayo kuti azikapereka nsembe kumeneko ndipo amange maziko olimba. Nyumbayo ikhale mikono 60* kupita mʼmwamba ndiponso mikono 60 mulifupi mwake.+ 4 Ikhale ndi mizere itatu yamiyala ikuluikulu yochita kugubuduza komanso mzere umodzi wa matabwa.+ Ndalama zake zichokere kunyumba ya mfumu.+
-