-
Deuteronomo 12:29, 30Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
29 Yehova Mulungu wanu akadzawononga mitundu imene mukupita kukailanda dziko,+ inuyo nʼkuyamba kukhala mʼdziko lawolo, 30 mukasamale kuti musakagwidwe mumsampha wawo, pambuyo poti awonongedwa ndi kuchotsedwa pamaso panu. Musakafunse zokhudza milungu yawo kuti, ‘Kodi mitundu imeneyi inkatumikira bwanji milungu yawo? Inenso ndichita zomwezo.’+
-