22 Aisiraeli anapitiriza kuyenda mʼmachimo onse amene Yerobowamu anachita.+ Sanawasiye 23 mpaka Yehova anachotsa Aisiraeli pamaso pake ngati mmene ananenera kudzera mwa atumiki ake onse, aneneri.+ Choncho Aisiraeli anatengedwa mʼdziko lawo nʼkupita nawo ku Asuri+ ndipo ali komweko mpaka lero.