-
Ezara 1:1-3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
1 Mʼchaka choyamba cha Koresi+ mfumu ya Perisiya, pokwaniritsa mawu a Yehova amene analankhula kudzera mwa Yeremiya,+ Yehova analimbikitsa Koresi mfumu ya Perisiya kuti alengeze mu ufumu wake wonse, zomwenso iye analemba mʼmakalata,+ kuti:
2 “Koresi mfumu ya Perisiya wanena kuti, ‘Yehova Mulungu wakumwamba wandipatsa maufumu onse apadziko lapansi.+ Iye wandituma kuti ndimumangire nyumba ku Yerusalemu+ mʼdziko la Yuda. 3 Aliyense amene ali pakati panu mwa anthu onse amene amamutumikira, Mulungu wake akhale naye ndipo apite ku Yerusalemu mʼdziko la Yuda nʼkukamanganso nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli. Iye ndi Mulungu woona ndipo nyumba yake inali ku Yerusalemu.*
-