3Ndiyeno Eliyasibu+ mkulu wa ansembe ndi abale ake, ansembe, anayamba kumanga Geti la Nkhosa+ ndipo analiyeretsa+ nʼkuika zitseko zake. Anayeretsa chigawo chonse mpaka ku Nsanja ya Meya+ nʼkukafika ku Nsanja ya Hananeli.+
13 Hanuni ndi anthu a ku Zanowa+ anakonza Geti la Kuchigwa.+ Iwo analikonza nʼkuika zitseko, anamphatika ndi mipiringidzo. Anakonzanso mpandawo mikono 1,000* mpaka kukafika ku Geti la Milu ya Phulusa.+