Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mafumu 24:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Yehoyakini mfumu ya Yuda anapita kwa mfumu ya Babulo+ pamodzi ndi mayi ake, atumiki ake, akalonga ake ndi nduna za panyumba yake+ ndipo mfumu ya Babuloyo inamutenga nʼkupita naye ku ukapolo mʼchaka cha 8 cha ufumu wake.+

  • 2 Mafumu 24:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Mfumuyo inatenga anthu onse a ku Yerusalemu, akalonga onse,+ asilikali onse amphamvu, amisiri onse ndiponso anthu osula zitsulo*+ nʼkupita nawo ku Babulo. Anthu onse amene inawatenga analipo 10,000. Palibe amene anatsala, kupatulapo anthu osauka kwambiri a mʼdzikolo.+

  • 2 Mbiri 36:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Choncho anawabweretsera mfumu ya Akasidi+ yomwe inapha anyamata awo ndi lupanga+ mʼnyumba yopatulika.+ Sinamvere chisoni mnyamata kapena namwali, wachikulire kapena wodwala.+ Mulungu anapereka zonse mʼmanja mwake.+

  • 2 Mbiri 36:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Nebukadinezara anatenga anthu amene sanaphedwe ndi lupanga+ nʼkupita nawo ku Babulo. Anthuwo anakhala antchito ake+ ndiponso a ana ake mpaka pamene ufumu wa Perisiya unayamba kulamulira.+

  • Yeremiya 39:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu, anatenga anthu ena onse otsala mumzindamo, anthu amene anathawira kwa mfumu ya Babulo ndi anthu ena onse amene anapulumuka nʼkupita nawo ku ukapolo ku Babulo.

  • Yeremiya 52:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu anatenga ena mwa anthu onyozeka ndiponso anthu ena onse amene anatsala mumzindawo. Anatenganso anthu amene anathawira kwa mfumu ya Babulo komanso amisiri onse aluso nʼkupita nawo ku ukapolo.+

  • Yeremiya 52:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Chiwerengero cha anthu amene Nebukadinezara* anawatenga kupita nawo ku ukapolo ndi ichi: mʼchaka cha 7 cha ulamuliro wake, anatenga Ayuda 3,023.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena