-
2 Samueli 17:27-29Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Davide atangofika ku Mahanaimu, Sobi mwana wamwamuna wa Nahasi wochokera ku Raba+ mzinda wa Aamoni, Makiri+ mwana wa Amiyeli wochokera ku Lo-debara komanso Barizilai+ wa ku Giliyadi wochokera ku Rogelimu, 28 anabweretsa mabedi, mabeseni, miphika, tirigu, balere, ufa, nyemba zikuluzikulu, mphodza, mbewu zina zokazinga, 29 uchi, nkhosa, bata ndiponso tchizi.* Anabweretsa zinthu zimenezi kuti Davide ndi anthu onse amene anali naye adye.+ Iwo ankati: “Anthuwa ali mʼchipululu ndipo ali ndi njala, ali ndi ludzu komanso atopa.”+
-