Ekisodo 15:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Pamene amuna ankaimba, Miriamu ankathirira mangʼombe kuti: “Imbirani Yehova chifukwa walemekezeka kwambiri.+ Mahatchi ndi okwera pamahatchiwo wawaponyera mʼnyanja.”+ 1 Samueli 18:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Davide ndi asilikali ena akamabwera kuchokera kokapha Afilisiti, azimayi ankatuluka mʼmizinda yonse ya Isiraeli akuimba nyimbo+ komanso kuvina. Iwo ankapita kukachingamira Mfumu Sauli mosangalala, akuimba maseche+ komanso choimbira cha zingwe zitatu.
21 Pamene amuna ankaimba, Miriamu ankathirira mangʼombe kuti: “Imbirani Yehova chifukwa walemekezeka kwambiri.+ Mahatchi ndi okwera pamahatchiwo wawaponyera mʼnyanja.”+
6 Davide ndi asilikali ena akamabwera kuchokera kokapha Afilisiti, azimayi ankatuluka mʼmizinda yonse ya Isiraeli akuimba nyimbo+ komanso kuvina. Iwo ankapita kukachingamira Mfumu Sauli mosangalala, akuimba maseche+ komanso choimbira cha zingwe zitatu.