8 Awa ndi mayina a atsogoleri a nyumba za makolo awo komanso mndandanda wa mayina wotsatira makolo a anthu amene ndinachoka nawo ku Babulo, mu ulamuliro wa Mfumu Aritasasita:+ 2 Pa ana a Pinihasi+ panali Gerisomu, pa ana a Itamara+ panali Danieli, pa ana a Davide panali Hatusi.