Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Nehemiya 10:35-37
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 Tinalonjezanso kuti chaka chilichonse tizibweretsa kunyumba ya Yehova zipatso zoyambirira kupsa zamʼdziko lathu komanso za mtengo uliwonse.+ 36 Tizibweretsanso ana athu aamuna oyamba kubadwa ndiponso a ziweto zathu+ mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼChilamulo. Tizibweretsa ana oyamba kubadwa a ngʼombe ndi nkhosa zathu. Tizibweretsa zimenezi kunyumba ya Mulungu wathu, kwa ansembe amene amatumikira mʼnyumba ya Mulungu wathu.+ 37 Komanso tizibweretsa ufa woyambirira wamisere,+ zopereka zathu, zipatso za mtengo uliwonse,+ vinyo watsopano ndi mafuta+ kwa ansembe mʼzipinda zosungira katundu* mʼnyumba ya Mulungu wathu.+ Tifunikanso kubweretsa chakhumi kwa Alevi pa zinthu zochokera mʼdziko lathu+ chifukwa Aleviwo ndi amene amatolera chakhumi kuchokera mʼmizinda yathu yonse ya zaulimi.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena