-
Nehemiya 10:37, 38Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
37 Komanso tizibweretsa ufa woyambirira wamisere,+ zopereka zathu, zipatso za mtengo uliwonse,+ vinyo watsopano ndi mafuta+ kwa ansembe mʼzipinda zosungira katundu* mʼnyumba ya Mulungu wathu.+ Tifunikanso kubweretsa chakhumi kwa Alevi pa zinthu zochokera mʼdziko lathu+ chifukwa Aleviwo ndi amene amatolera chakhumi kuchokera mʼmizinda yathu yonse ya zaulimi.
38 Wansembe, mwana wamwamuna wa Aroni, azikhala ndi Alevi pamene iwo akutolera chakhumi. Aleviwo azipereka gawo limodzi pa magawo 10 a chakhumicho kunyumba ya Mulungu wathu+ kuzipinda* za nyumba yosungira katundu.
-