14 Mukamapereka kwa Yehova nsembe yambewu ya zipatso zoyambirira kucha, muzipereka tirigu watsopano wokazinga pamoto, wosinja kuti akhale nsembe yambewu ya zipatso zanu zoyambirira kucha.+ 15 Muzithira mafuta ndi kuika lubani pansembeyo. Imeneyi ndi nsembe yambewu.