12 ndikupatsa zimene wapempha.+ Ndikupatsa mtima wanzeru ndi womvetsa zinthu+ kuposa anthu onse amene anakhalapo mʼmbuyomu komanso amene adzakhaleko mʼtsogolo.+ 13 Ndikupatsanso zomwe sunapemphe.+ Ndikupatsa chuma ndi ulemerero,+ moti sikudzakhalanso mfumu ngati iwe pa nthawi yonse ya moyo wako.+