2 Kenako Sekaniya mwana wa Yehiela+ wochokera mwa ana a Elamu+ anauza Ezara kuti: “Ifeyo tachita zosakhulupirika kwa Mulungu wathu chifukwa tinakwatira akazi achilendo kuchokera kwa anthu a mitundu ina.+ Ngakhale zili choncho, Aisiraeli ali ndi chiyembekezo.