-
Yakobo 1:10, 11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 ndipo wachuma asangalale chifukwa waphunzira kukhala wodzichepetsa,+ chifukwa mofanana ndi duwa lakutchire, iye adzafota. 11 Dzuwa likatuluka limatentha kwambiri nʼkufotetsa zomera ndipo maluwa a zomerazo amathothoka moti kukongola kwake kumatha. Mofanana ndi zimenezi munthu wachumayo adzafa ali mkati mofunafuna chuma.+
-
-
1 Petulo 1:24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Pakuti “anthu onse ali ngati udzu, ndipo ulemerero wawo wonse uli ngati duwa lakutchire. Udzu umafota ndipo duwa limathothoka,
-