Luka 23:42 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 42 Kenako ananena kuti: “Yesu, mukandikumbukire mukakalowa mu Ufumu wanu.”+ Yohane 5:28, 29 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 Musadabwe nazo zimenezi, chifukwa nthawi ikubwera imene onse amene ali mʼmanda achikumbutso adzamva mawu ake+ 29 ndipo adzatuluka. Amene ankachita zabwino adzauka kuti alandire moyo ndipo amene ankachita zoipa adzauka kuti aweruzidwe.+ Aheberi 11:35 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 35 Akazi analandira anthu akufa amene anaukitsidwa.+ Koma anthu ena anazunzidwa chifukwa sanalole kusiya chikhulupiriro chawo kuti amasulidwe. Iwo anachita zimenezi kuti adzaukitsidwe pa kuuka kwabwino kwambiri.
28 Musadabwe nazo zimenezi, chifukwa nthawi ikubwera imene onse amene ali mʼmanda achikumbutso adzamva mawu ake+ 29 ndipo adzatuluka. Amene ankachita zabwino adzauka kuti alandire moyo ndipo amene ankachita zoipa adzauka kuti aweruzidwe.+
35 Akazi analandira anthu akufa amene anaukitsidwa.+ Koma anthu ena anazunzidwa chifukwa sanalole kusiya chikhulupiriro chawo kuti amasulidwe. Iwo anachita zimenezi kuti adzaukitsidwe pa kuuka kwabwino kwambiri.