-
Yobu 1:10-12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Kodi inuyo simwamuteteza pomuikira mpanda?+ Mwatetezanso nyumba yake ndi zinthu zonse zimene ali nazo. Mwadalitsa ntchito ya manja ake+ ndipo ziweto zake zachuluka kwambiri mʼdzikoli. 11 Koma panopa mutambasule dzanja lanu nʼkuwononga zinthu zonse zimene ali nazo, ndipo muona, akutukwanani mʼmaso muli gwa!” 12 Kenako Yehova anauza Satana kuti: “Chabwino, chilichonse chimene ali nacho chili mʼmanja mwako. Koma dzanja lako lisakhudze munthuyo.” Zitatero Satana anachoka pamaso pa Yehova.+
-