4 Mayi wina yemwe anali mmodzi wa akazi a ana a aneneri,+ anauza Elisa modandaula kuti: “Mtumiki wanu yemwe anali mwamuna wanga anamwalira ndipo inu mukudziwa bwino kuti ankaopa Yehova.+ Tsopano kwabwera wangongole kudzatenga ana anga onse awiri kuti akakhale akapolo ake.”