22 Zonsezi mfundo yake ndi imodzi. Nʼchifukwa chake ndikunena kuti,
‘Iye amawononga onse, osalakwa komanso oipa.’
23 Anthu atafa mwadzidzidzi ndi madzi osefukira,
Iye angaseke anthu osalakwa akuvutika.
24 Dziko lapansi laperekedwa mʼmanja mwa anthu oipa.+
Iye amaphimba maso a oweruza a dzikolo.
Ngati si iyeyo, ndiye ndi ndani?