-
Yesaya 51:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 “Ineyo ndi amene ndikukutonthoza.+
Ndiye nʼchifukwa chiyani ukuopa munthu woti adzafa+
Ndiponso mwana wa munthu amene adzanyale ngati udzu wobiriwira?
13 Nʼchifukwa chiyani ukuiwala Yehova amene anakupanga,+
Amene anatambasula kumwamba+ ndi kuyala maziko a dziko lapansi?
Ndipo tsiku lonse unkangokhalira kuopa mkwiyo wa amene amakupondereza,
Ngati kuti ali ndi mphamvu zoti akanatha kukuwononga.
Kodi tsopano mkwiyo wa amene ankakupondereza uja uli kuti?
-