16 Pa nthawi imeneyi mʼpamene amatsegula anthu makutu,+
Ndipo amadinda malangizo ake mʼmaganizo mwawo,
17 Pofuna kubweza munthu kuti asachite zoipa+
Komanso kumuteteza kuti asakhale wonyada.+
18 Mulungu amateteza moyo wake kuti usapite kudzenje,+
Amateteza munthu kuti asawonongedwe ndi lupanga.