-
Genesis 12:6, 7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Abulamu anadutsa mʼdzikolo mpaka kukafika ku Sekemu,+ pafupi ndi mitengo ikuluikulu ya ku More.+ Pa nthawiyo nʼkuti Akanani akukhala mʼdzikomo. 7 Ndiyeno Yehova anaonekera kwa Abulamu nʼkumuuza kuti: “Ndidzapereka dziko ili+ kwa mbadwa* zako.”+ Choncho Abulamu anamanga guwa lansembe pamalo amene Yehova anaonekera kwa iye.
-