4 Yehova, pamene munayenda kuchokera ku Seiri,+
Pamene munaguba kuchokera kudera la Edomu,
Dziko linagwedezeka ndipo kumwamba kunagwetsa madzi,
Mitambo inagwetsa madzi.
5 Mapiri anasungunuka pamaso pa Yehova,+
Ngakhalenso Sinai anasungunuka pamaso pa Yehova,+ Mulungu wa Isiraeli.+