Salimo 22:9, 10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Inu ndi amene munanditulutsa mʼmimba,+Ndinu amene munandichititsa kumva kuti ndine wotetezeka pamene ndinkayamwa mabere a mayi anga. 10 Ndinaperekedwa kwa inu kuti muzindisamalira* kuyambira pamene ndinabadwa.Kuyambira ndili mʼmimba mwa mayi anga, inu mwakhala Mulungu wanga. Salimo 139:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Maso anu anandiona ngakhale pamene ndinali mluza.*Ziwalo zanga zonse zinalembedwa mʼbuku lanuMʼbukumo munalembedwa za masiku amene zinapangidwa,Zinalembedwa chiwalo chilichonse chisanapangidwe. Yesaya 46:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 “Inu anyumba ya Yakobo ndimvetsereni, komanso inu nonse otsala a mʼnyumba ya Isiraeli,+Inu amene ndakuthandizani kuyambira pamene munabadwa ndiponso kukunyamulani kuyambira pamene munatuluka mʼmimba.+
9 Inu ndi amene munanditulutsa mʼmimba,+Ndinu amene munandichititsa kumva kuti ndine wotetezeka pamene ndinkayamwa mabere a mayi anga. 10 Ndinaperekedwa kwa inu kuti muzindisamalira* kuyambira pamene ndinabadwa.Kuyambira ndili mʼmimba mwa mayi anga, inu mwakhala Mulungu wanga.
16 Maso anu anandiona ngakhale pamene ndinali mluza.*Ziwalo zanga zonse zinalembedwa mʼbuku lanuMʼbukumo munalembedwa za masiku amene zinapangidwa,Zinalembedwa chiwalo chilichonse chisanapangidwe.
3 “Inu anyumba ya Yakobo ndimvetsereni, komanso inu nonse otsala a mʼnyumba ya Isiraeli,+Inu amene ndakuthandizani kuyambira pamene munabadwa ndiponso kukunyamulani kuyambira pamene munatuluka mʼmimba.+