-
1 Mafumu 10:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Mfumukazi ya ku Sheba inamva za Solomo, zoti anatchuka chifukwa cha dzina la Yehova.+ Choncho inabwera kuti idzamuyese pomufunsa mafunso ovuta.+ 2 Mfumukaziyo inafika ku Yerusalemu ndi anthu ambiri oiperekeza.+ Inabwera ndi ngamila zitanyamula mafuta a basamu,+ golide wambiri ndi miyala yamtengo wapatali. Inafika kwa Solomo nʼkuyamba kulankhula naye zonse zimene zinali mumtima mwake.
-