13 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, “Ine ndikukuukira.+
Nditentha magaleta ako ankhondo mpaka akhala phulusa.+
Ndipo lupanga lidzapha mikango yako yamphamvu.
Ndidzachititsa kuti usagwirenso nyama padziko lapansi,
Ndipo mawu a anthu amene umawatuma kukanena uthenga sadzamvekanso.”+