-
Yesaya 63:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Iwo anakumbukira masiku akale,
Masiku a Mose mtumiki wake,
Ndipo anafunsa kuti: “Kodi amene anawatulutsa mʼnyanja+ pamodzi ndi abusa a anthu ake+ uja ali kuti?
Ali kuti amene anaika mzimu wake woyera mwa iye?+
-
Machitidwe 7:35, 36Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
35 Mose yemweyo, amene iwo anamukana nʼkunena kuti, ‘Ndani anakupatsa udindo woti uzitilamulira komanso kutiweruza?’+ ndi amene Mulungu anamutumiza+ ngati wolamulira ndi mpulumutsi kudzera mwa mngelo amene anaonekera kwa iye pachitsamba chaminga chija. 36 Munthu ameneyo anawatsogolera nʼkutuluka nawo+ ndipo anachita zodabwitsa ndi zizindikiro ku Iguputo,+ pa Nyanja Yofiira+ ndiponso mʼchipululu kwa zaka 40.+
-
-
-