20 Mtambowo unaima pakati pa Aiguputo ndi Aisiraeli.+ Mbali imodzi unkachititsa mdima, ndipo mbali ina unkawaunikira usiku.+ Choncho gulu la Aiguputo silinayandikire gulu la Aisiraeli usiku wonse.
24 Ndiyeno chakumʼbandakucha,* Yehova ali mʼchipilala cha mtambo ndi cha moto chija,+ anayangʼana gulu la Aiguputo ndipo anachititsa kuti Aiguputowo asokonezeke.