15 Yangʼanani muli kumwamba ndipo muone
Kuchokera pamalo anu okhala apamwamba, oyera ndi aulemerero.
Kodi mtima wanu wodzipereka kwambiri ndiponso mphamvu zanu zili kuti?
Kodi chikondi chanu chachikulu+ ndi chifundo chanu+ zili kuti?
Chifukwa simukundisonyezanso zimenezi.