2 Choncho Yehova anawapereka* kwa Yabini mfumu ya ku Kanani,+ amene ankalamulira ku Hazori. Mkulu wa gulu lake lankhondo anali Sisera, ndipo ankakhala ku Haroseti-ha-goimu.+
7 Ine ndidzabweretsa kwa iwe kumtsinje* wa Kisoni,+ Sisera mkulu wa gulu lankhondo la Yabini, pamodzi ndi magaleta ake ankhondo ndi asilikali ake ndipo ndidzamʼpereka mʼmanja mwako.’”+