-
Machitidwe 2:25-28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Paja Davide ananena za iyeyu kuti, ‘Ndimaika Yehova* patsogolo panga nthawi zonse. Chifukwa iye ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka. 26 Pa chifukwa chimenechi mtima wanga unasangalala ndipo ndinalankhula mosangalala kwambiri. Komanso ine ndidzakhala ndi chiyembekezo, 27 chifukwa simudzandisiya* mʼManda,* ndipo simudzalola kuti thupi la wokhulupirika wanu livunde.*+ 28 Mwandidziwitsa njira za moyo, ndipo mudzachititsa kuti ndizisangalala kwambiri ndikakhala nanu pafupi.’*+
-