-
Genesis 1:29, 30Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
29 Kenako Mulungu anati: “Ndakupatsani zomera zonse zimene zili padziko lapansi zobereka mbewu komanso mitengo yonse yobereka zipatso zokhala ndi nthangala kuti zikhale chakudya chanu.+ 30 Ndapereka zomera zonse kuti zikhale chakudya+ cha nyama iliyonse yamʼtchire padziko lapansi, chamoyo chilichonse chouluka mumlengalenga komanso chokwawa chilichonse chapadziko lapansi chimene chili ndi moyo.” Ndipo zinaterodi.
-