Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 3:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Udzadya chakudya kuchokera mʼthukuta la nkhope yako mpaka utabwerera kunthaka, chifukwa nʼkumene unatengedwa.+ Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwerera.”+

  • Yobu 34:14, 15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Iye akakwiyira anthu,

      Nʼkutenga mphamvu ya moyo* komanso mpweya wawo,+

      15 Anthu onse amafera limodzi,

      Ndipo anthuwo amabwerera kufumbi.+

  • Salimo 146:3, 4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Musamakhulupirire anthu olemekezeka*

      Kapena mwana wa munthu amene sangabweretse chipulumutso.+

       4 Mpweya* wake umachoka, ndipo iye amabwerera kunthaka.+

      Pa tsiku limenelo zonse zimene amaganiza zimatheratu.+

  • Mlaliki 3:19, 20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Chifukwa anthu ali ndi mapeto ndipo nyamanso zili ndi mapeto. Mapeto a zonsezi ndi ofanana.+ Nyama imafa ndipo munthunso amafa, zonsezi zili ndi mzimu wofanana.+ Choncho munthu saposa nyama, chifukwa zinthu zonse nʼzachabechabe. 20 Zonse zimapita kumalo amodzi.+ Zonse zinachokera kufumbi+ ndipo zonse zimabwerera kufumbi.+

  • Mlaliki 12:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Kenako fumbi lidzabwerera kunthaka+ kumene linali, ndipo mzimu* udzabwerera kwa Mulungu woona amene anaupereka.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena