8 “Yamikani Yehova,+ itanani pa dzina lake,
Dziwitsani mitundu ya anthu ntchito zake!+
9 Muimbireni, muimbireni nyimbo zomutamanda,+
Ganizirani mozama ntchito zake zonse zodabwitsa.+
10 Nyadirani dzina lake loyera.+
Mitima ya anthu ofunafuna Yehova isangalale.+
11 Funafunani Yehova+ ndipo muzidalira mphamvu zake.
Nthawi zonse muzimupempha kuti akuthandizeni.+
12 Kumbukirani ntchito zodabwitsa zimene wachita,+
Kumbukirani zozizwitsa zake ndi ziweruzo zimene wanena,
13 Inu mbadwa za Isiraeli mtumiki wake,+
Inu ana a Yakobo, osankhidwa ake.+