-
1 Mbiri 16:14-18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Iye ndi Yehova Mulungu wathu.+
Ziweruzo zake zili padziko lonse lapansi.+
15 Kumbukirani pangano lake mpaka kalekale,
Lonjezo limene anapereka ku mibadwo 1,000,+
16 Kumbukirani pangano limene anapangana ndi Abulahamu,+
Komanso lumbiro limene analumbira kwa Isaki.+
17 Pangano limene analikhazikitsa monga lamulo kwa Yakobo,+
Komanso monga pangano lokhalapo mpaka kalekale kwa Isiraeli,
18 Pamene anati: ‘Ndidzakupatsa dziko la Kanani,+
Kuti likhale cholowa chako.’+
-