Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 12:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Ndiyeno Yehova anaonekera kwa Abulamu nʼkumuuza kuti: “Ndidzapereka dziko ili+ kwa mbadwa* zako.”+ Choncho Abulamu anamanga guwa lansembe pamalo amene Yehova anaonekera kwa iye.

  • Genesis 13:14, 15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Abulamu atasiyana ndi Loti, Yehova anamuuza kuti: “Takweza maso ako kuchokera pamene ulipo. Uyangʼane kumpoto ndi kumʼmwera, komanso kumʼmawa ndi kumadzulo. 15 Dziko lonse limene ukulionali, ndidzalipereka kwa iwe ndi kwa mbadwa zako,* kuti likhale lanu mpaka kalekale.+

  • Genesis 15:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Pa tsiku limeneli Yehova anachita pangano ndi Abulamu+ kuti: “Dziko ili ndidzalipereka kwa mbadwa* zako,+ kuyambira kumtsinje wa ku Iguputo mpaka kumtsinje waukulu, mtsinje wa Firate.+

  • Genesis 26:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Ukhale ngati mlendo mʼdzikoli,+ ndipo ndidzapitiriza kukhala nawe ndi kukudalitsa, chifukwa mayiko onsewa ndidzawapereka kwa iwe ndi kwa mbadwa* zako.+ Ndidzakwaniritsa lumbiro limene ndinalumbira kwa bambo ako Abulahamu+ kuti:

  • Genesis 28:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Pamwamba pa masitepewo anaonapo Yehova, amene anamuuza kuti:

      “Ine ndine Yehova, Mulungu wa Abulahamu kholo lako ndi Mulungu wa Isaki.+ Dziko limene wagonapoli ndidzalipereka kwa iwe ndi kwa mbadwa* zako.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena