Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 17:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Dziko limene ukukhalamo ngati mlendoli,+ ndidzalipereka kwa iwe ndi mbadwa zako. Dziko lonse la Kanani lidzakhala lawo mpaka kalekale, ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo.”+

  • Genesis 23:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 “Ine ndinadzakhala kwanu kuno ngati mlendo.+ Choncho mundipatseko malo kuti ndikhale ndi manda angaanga, ndiikemo mkazi wanga.”

  • 1 Mbiri 16:19-22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Pamene ankanena zimenezi nʼkuti inu mulipo ochepa,

      Nʼkuti mulipo ochepa kwambiri komanso muli alendo mʼdzikolo.+

      20 Iwo ankayendayenda kuchokera ku mtundu wina kupita ku mtundu wina,

      Komanso kuchokera mu ufumu wina kupita kwa anthu a mtundu wina.+

      21 Mulungu sanalole kuti munthu aliyense awapondereze,+

      Koma anadzudzula mafumu chifukwa cha iwo.+

      22 Iye anati: ‘Musakhudze odzozedwa anga,

      Ndipo aneneri anga musawachitire choipa chilichonse.’+

  • Machitidwe 7:4, 5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Choncho anasamuka mʼdziko la Akasidi nʼkukakhala ku Harana. Kumeneko, bambo ake atamwalira,+ Mulungu anamuuza kuti asamukire mʼdziko lino limene inu mukukhala panopa.+ 5 Koma sanamʼpatsemo cholowa chilichonse, ngakhale kadera kakangʼono. Mʼmalomwake anamulonjeza kuti adzamupatsa dzikoli kuti likhale cholowa chake, ndi cha mbadwa* zake,+ ngakhale kuti pa nthawiyo analibe mwana.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena