-
Ekisodo 7:20, 21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Nthawi yomweyo Mose ndi Aroni anachita mogwirizana ndi zimene Yehova anawalamula. Aroni anatenga ndodo yake nʼkumenya madzi amumtsinje wa Nailo, Farao ndi atumiki ake akuona ndipo madzi onse amumtsinje wa Nailo anasanduka magazi.+ 21 Zitatero nsomba zamumtsinje wa Nailo zinafa+ ndipo mtsinjewo unayamba kununkha. Aiguputo sanathenso kumwa madzi amumtsinje wa Nailo.+ Mʼdziko lonse la Iguputo munali magazi okhaokha.
-